Akwera ku Kachisi, ndi ku Diboni, kumisanje, kukalira; pa Nebo ndi pa Medeba a Mowabu pali kulira; pamitu pao ponse pali dazi, ndevu zonse zametedwa.
Yeremiya 48:3 - Buku Lopatulika Mau amveka kuchokera ku Horonaimu, kufunkha ndi kuononga kwakukulu! Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mau amveka kuchokera ku Horonaimu, kufunkha ndi kuononga kwakukulu! Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Imvani kulira kwachisoni kwa anthu a ku Horonaimu, akuti, ‘Chisakazo ndi chiwonongeko chachikulutu!’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tamvani mfuwu wa anthu a ku Horonaimu. Iwo akulira kuti, ‘Kusakazika ndi kuwonongeka kwakukulu.’ |
Akwera ku Kachisi, ndi ku Diboni, kumisanje, kukalira; pa Nebo ndi pa Medeba a Mowabu pali kulira; pamitu pao ponse pali dazi, ndevu zonse zametedwa.
Mtima wanga ufuula chifukwa cha Mowabu: akulu ake athawira ku Zowari, ku Egilati-Selisiya; pakuti pa chikweza cha Luhiti akwera alikulira, pakuti m'njira ya Horonaimu akweza mfuu wa chionongeko.
Pakuti kulira kwamveka kuzungulira malire a Mowabu; kukuwa kwake kwafikira ku Egilaimu, ndi kukuwa kwake kwafikira ku Beerelimu.
Chomwecho ndinati, Usandiyang'ane ine, ndilira ndi kuwawa mtima; usafulumire kunditonthoza ine, chifukwa cha kufunkhidwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga.
Munthuyo akhale ngati mizinda imene Yehova anapasula, osalekerera; amve mfuu mamawa, ndi mkuwo pausana;
Yehova atero: Taonani, madzi adzakwera kutuluka kumpoto, nadzakhala mtsinje wosefuka, nadzasefukira padziko ndi pa zonse zili m'mwemo, pamzinda ndi pa onse okhalamo; ndipo amuna adzalira, ndi onse okhala m'dziko adzakuwa.
Kuyambira kufuula kwa Hesiboni mpaka ku Eleyale, mpaka ku Yahazi anakweza mau, kuyambira pa Zowari mpaka ku Horonaimu, ku Egilati-Selisiya; pakuti pamadzi a ku Nimurimu komwe padzakhala mabwinja.
Pakuti adzakwera pa chikweza cha Luhiti ndi kulira kosaleka; pakuti pa chitsiko cha Horonaimu amva kulira kowawa kwa chionongeko.