amene mivi yao ili yakuthwa, ndi mauta ao onse athifuka; ziboda za akavalo ao zidzayesedwa ngati mwala, ndi njinga zao ngati kamvulumvulu;
Yeremiya 47:3 - Buku Lopatulika Pomveka migugu ya ziboda za olimba ake, pogumukira magaleta ake, ndi pophokosera njinga zake, atate sadzacheukira ana ao chifukwa cha kulefuka kwa manja ao; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomveka migugu ya ziboda za olimba ake, pogumukira magaleta ake, ndi pophokosera njinga zake, atate sadzacheukira ana ao chifukwa cha kulefuka kwa manja ao; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adzamva mgugu wa akavalo othamanga, adzamva phokoso la magaleta ake, ndi kulira kwa mikombero yake. Atate sadzaganizirako za ana ao, adzangokhala ali manja lende! Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero akadzamva mgugu wa ngʼombe zazimuna zothamanga, phokoso la magaleta ake ndi kulira kwa mikombero yake. Makolo sadzatembenuka kuti athandize ana awo; manja awo adzangoti khoba. |
amene mivi yao ili yakuthwa, ndi mauta ao onse athifuka; ziboda za akavalo ao zidzayesedwa ngati mwala, ndi njinga zao ngati kamvulumvulu;
Kwerani, inu akavalo; chitani misala, inu magaleta, atuluke amphamvu; Akusi ndi Aputi, ogwira chikopa; ndi Aludi, amene agwira ndi kukoka uta.
Agwira uta ndi nthungo; ali ankharwe, alibe chifundo; mau ao apokosera ngati nyanja, ndipo akwera akavalo, yense aguba monga munthu wa kunkhondo, kukamenyana ndi iwe, mwana wamkazi wa Babiloni.
Kumina kwa akavalo ake kunamveka ku Dani; dziko lonse linanthunthumira pa kulira kwa akavalo akewo olimba; chifukwa afika, nadya dziko ndi zonse za momwemo; mzinda ndi amene akhalamo.
Ndipo adzakudzera ndi zida, magaleta a nkhondo, ndi magaleta ena, pamodzi ndi msonkhano wa mitundu ya anthu; adzadziikira pozungulira pako ndi zikopa zotchinjiriza ndi zisoti; ndipo ndidzawaika aweruze, nadzakuweruza monga mwa maweruzo ao.
Magaleta achita mkokomo m'miseu, akankhana m'makwalala; maonekedwe ao akunga miuni, athamanga ngati mphezi.
Koma Ninive wakhala chiyambire chake ngati thamanda lamadzi; koma athawa. Imani, Imani! Ati, koma palibe wocheuka.
Ndipo anali nazo zikopa ngati zikopa zachitsulo; ndipo mkokomo wa mapiko ao ngati mkokomo wa agaleta, a akavalo ambiri akuthamangira kunkhondo.
Pamenepo ziboda za akavalo zinaguguda. Ndi kutumphatumpha, kutumphatumpha kwa anthu ake eni mphamvu.