Koma kunali mwezi wachisanu ndi chiwiri anadza Ismaele mwana wa Netaniya mwana wa Elisama, wa mbumba yachifumu, ndi anthu khumi pamodzi naye, nakantha Gedaliya; nafa iye, ndi Ayuda, ndi Ababiloni okhala naye ku Mizipa.
Yeremiya 41:3 - Buku Lopatulika Ismaele naphanso Ayuda onse okhala naye Gedaliya pa Mizipa, ndi Ababiloni amene anakomana nao komweko, amuna a nkhondo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ismaele naphanso Ayuda onse okhala naye Gedaliya pa Mizipa, ndi Ababiloni amene anakomana nao komweko, amuna a nkhondo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ismaele adaphanso Ayuda onse amene anali ku Mizipa ndiponso ankhondo a Ababiloni amene anali kumeneko. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ismaeli anaphanso Ayuda onse amene anali pamodzi ndi Gedaliya ku Mizipa, kuphatikizanso asilikali a Ababuloni amene anali ku Mizipako. |
Koma kunali mwezi wachisanu ndi chiwiri anadza Ismaele mwana wa Netaniya mwana wa Elisama, wa mbumba yachifumu, ndi anthu khumi pamodzi naye, nakantha Gedaliya; nafa iye, ndi Ayuda, ndi Ababiloni okhala naye ku Mizipa.
Ndipo anauka Ismaele mwana wa Netaniya, ndi anthu khumi okhala naye, namkantha Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani ndi lupanga, namupha iye, amene mfumu ya ku Babiloni inamuika wolamulira dziko.
Uliralira usiku; misozi yake ili pa masaya ake; mwa onse amene anaukonda mulibe mmodzi wakuutonthoza: Mabwenzi ake onse auchitira ziwembu, asanduka adani ake.