Pakuti Yehova wa makamu, amene anakuoka iwe, wakunenera iwe choipa, chifukwa cha zoipa za nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda, zimene anadzichitira okha pakuutsa mkwiyo wanga m'mene anafukizira Baala.
Yeremiya 40:2 - Buku Lopatulika Ndipo kapitao wa alonda anatenga Yeremiya, nati kwa iye, Yehova Mulungu wako ananenera choipa ichi malo ano; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kapitao wa alonda anatenga Yeremiya, nati kwa iye, Yehova Mulungu wako ananenera choipa ichi malo ano; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mtsogoleriyo adatenga Yeremiya namuuza kuti, “Chauta, Mulungu wako, adanena kuti adzaononga malo ano. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mtsogoleriyu anamupeza Yeremiya, anamuwuza kuti, “Yehova Mulungu wako analengeza kale zakuti malo ano adzawonongedwa. |
Pakuti Yehova wa makamu, amene anakuoka iwe, wakunenera iwe choipa, chifukwa cha zoipa za nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda, zimene anadzichitira okha pakuutsa mkwiyo wanga m'mene anafukizira Baala.
Onse amene anazipeza anazidya; adani ao anati, Sitipalamula mlandu, chifukwa iwo anachimwira Yehova, ndiye mokhalamo zolungama, Yehova, chiyembekezo cha atate ao.
Koma Nebuzaradani kapitao wa alonda anasiya aumphawi a padziko akhale akulima mphesa ndi akulima m'minda.
Koma kudzali, mukapanda kumvera mau a Yehova Mulungu wanu, kusamalira kuchita malamulo ake onse ndi malemba ake amene ndikuuzani lero, kuti matemberero awa onse adzakugwerani ndi kukupezani.
Pamenepo ndidzawapsera mtima tsiku ilo, ndipo ndidzawataya, ndi kuwabisira nkhope yanga, ndipo adzathedwa, ndi zoipa ndi zovuta zambiri zidzawafikira; kotero kuti adzati tsiku lija, Sizitifikira kodi zoipa izi popeza Mulungu wathu sakhala pakati pa ife?