Dziko lapansi ndipo linali lopasuka ndi losoweka; ndipo mdima unali pamwamba panyanja; ndipo mzimu wa Mulungu unalinkufungatira pamwamba pamadzi.
Yeremiya 4:23 - Buku Lopatulika Ndinaona dziko lapansi, ndipo taona, linali lopasuka lopanda kanthu; ndipo ndinaona kumwamba, kunalibe kuunika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndinaona dziko lapansi, ndipo taona, linali lopasuka lopanda kanthu; ndipo ndinaona kumwamba, kunalibe kuunika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidayang'ana dziko lapansi, linali lopanda anthu ndi lopanda kanthu kalikonse. Ndidayang'ana thambo, linalibe konse kuŵala. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndinayangʼana dziko lapansi, ndipo linali lopanda anthu ndi lopanda kanthu; ndinayangʼana thambo, koma linalibe kuwala kulikonse. |
Dziko lapansi ndipo linali lopasuka ndi losoweka; ndipo mdima unali pamwamba panyanja; ndipo mzimu wa Mulungu unalinkufungatira pamwamba pamadzi.
Chifukwa nyenyezi za kumwamba ndi makamu ao sizidzawala; dzuwa lidzada m'kutuluka kwake, ndipo mwezi sudzaonetsa kuwala kwake.
Ndipo iwo adzawabangulira tsiku limenelo ngati kukokoma kwa nyanja; ndipo wina ayang'ana padziko, taonani mdima ndi nsautso, kuyera kwadetsedwanso m'mitambo yake.
Chifukwa cha mapiri ndidzagwa misozi ndi kulira, chifukwa cha mabusa a chipululu ndidzachita maliro, chifukwa apserera, kuti anthu sangathe kupitirirapo; ndiponso anthu sangathe kumva mau a ng'ombe zao; mbalame za mlengalenga ndi nyama zathawa, zapita.
Dziko lapansi linjenjemera pamaso pao, thambo ligwedezeka, dzuwa ndi mwezi zada, ndi nyenyezi zibweza kuwala kwao;
Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, ati Ambuye Yehova, ndidzalowetsa dzuwa usana, ndi kudetsa dziko pausana poyera.
Koma pomwepo, atapita masauko a masiku awo, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzaonetsa kuwala kwake, ndi nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndi mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka:
Ndipo ndinaona, mpando wachifumu waukulu woyera, ndi Iye wakukhalapo, amene dziko ndi m'mwamba zinathawa pamaso pake, ndipo sanapezedwe malo ao.