Zedekiya anali wa zaka makumi awiri mphambu chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka khumi ndi chimodzi,
Yeremiya 32:1 - Buku Lopatulika Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova chaka chakhumi cha Zedekiya mfumu ya Yuda, chimene chinali chaka chakhumi ndi chisanu ndi chitatu cha Nebukadinezara. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova chaka chakhumi cha Zedekiya mfumu ya Yuda, chimene chinali chaka chakhumi ndi chisanu ndi chitatu cha Nebukadinezara. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adalankhula ndi Yeremiya pa chaka cha khumi cha ufumu wa Zedekiya ku Yuda, chimene chinali chaka cha 18 cha ufumu wa Nebukadinezara. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova anayankhula ndi Yeremiya mʼchaka chakhumi cha Zedekiya mfumu ya Yuda, chimene chinalinso chaka cha 18 cha ulamuliro wa Nebukadinezara. |
Zedekiya anali wa zaka makumi awiri mphambu chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka khumi ndi chimodzi,
Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, pamene Zedekiya mfumu anatuma kwa iye Pasuri mwana wa Malikiya, ndi Zefaniya mwana wake wa Maaseiya wansembe, akati,
Mau amene anadza kwa Yeremiya za anthu onse a Yuda chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda; ndicho chaka choyamba cha Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni;
Poyamba kukhala mfumu Zedekiya mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, mau awa anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, kuti,
Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, pamene Nebukadinezara mfumu ya Babiloni, ndi nkhondo yake yonse, ndi maufumu onse a dziko lapansi amene anagwira mwendo wake, ndi anthu onse, anamenyana ndi Yerusalemu, ndi mizinda yake yonse, akuti,
chaka chakhumi ndi chisanu ndi chitatu cha Nebukadinezara iye anatenga ndende kuchokera mu Yerusalemu anthu mazana asanu ndi atatu kudza makumi atatu ndi awiri;