Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Yeremiya 26:6 - Buku Lopatulika

pamenepo ndidzayesa nyumba iyi ifanane ndi Silo, ndipo ndidzayesa mzinda uwu chitemberero cha kwa mitundu yonse ya dziko lapansi.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

pamenepo ndidzayesa nyumba iyi ifanane ndi Silo, ndipo ndidzayesa mudzi uwu chitemberero cha kwa mitundu yonse ya dziko lapansi.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

ndiye kuti Nyumba ino ndidzaiwononga monga m'mene ndidaonongera Silo. Ndipo mzinda uno ndidzausandutsa chinthu chonyozeka kwa mitundu yonse ya pa dziko lapansi!”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

ndiye kuti Ine ndidzasandutsa Nyumba ino kukhala ngati Silo ndipo mzinda uno udzakhala chinthu chotembereredwa pakati pa mitundu yonse ya pa dziko lapansi.’ ”

Onani mutuwo



Yeremiya 26:6
20 Mawu Ofanana  

popeza mtima wako ngoolowa, ndipo unadzichepetsa pamaso pa Yehova muja udamva zonenera Ine malo ano ndi anthu okhalamo, kuti adzakhala abwinja, ndi temberero; ndipo unang'amba zovala zako ndi kulira misozi pamaso panga, Inenso ndakumvera, ati Yehova.


Chifukwa chake ndidzaipitsa akulu a Kachisi, ndipo ndidzasanduliza Yakobo akhale temberero, ndi Israele akhale chitonzo.


Ndipo mudzasiya dzina lanu likhale chitemberero kwa osankhidwa anga, ndipo Ambuye Yehova adzakupha iwe, nadzatcha atumiki ake dzina lina;


Ndipo ndidzawapatsa akhale choopsetsa choipa ku maufumu a dziko lapansi; akhale chitonzo ndi nkhani ndi choseketsa, ndi chitemberero, monse m'mene ndidzawapirikitsiramo.


Yerusalemu, ndi mizinda ya Yuda, ndi mafumu ake omwe, ndi akulu ake, kuwayesa iwo bwinja, chizizwitso, chotsonyetsa, ndi chitemberero; monga lero lino;


Ndipo ndidzatsata iwe ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri, ndipo ndidzawapereka akhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko lapansi, akhale chitemberero, ndi chodabwitsa, ndi chotsonyetsa, ndi chitonzo, kwa mitundu yonse kumene ndinawapirikitsirako;


ndipo am'nsinga onse a Yuda amene ali mu Babiloni adzatemberera pali iwo, kuti, Yehova akuchitire iwe monga Zedekiya ndi Ahabu, amene mfumu ya ku Babiloni inaotcha m'moto;


Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Monga mkwiyo wanga ndi ukali wanga wathiridwa kwa okhala mu Yerusalemu, momwemo ukali wanga udzathiridwa pa inu, pamene mudzalowa mu Ejipito; ndipo mudzakhala chitukwano, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, ndi chitonzo; ndipo simudzaonananso malo ano.


Ndipo Yehova sanathe kupirirabe, chifukwa cha machitidwe anu oipa, ndi chifukwa cha zonyansa zimene munazichita; chifukwa chake dziko lanu likhala bwinja, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, lopanda wokhalamo, monga lero lomwe.


Onse opita panjira akuombera manja: Atsonya, napukusira mitu yao pa mwana wamkazi wa Yerusalemu, nati, kodi uwu ndi mzinda wotchedwa wokongola, wangwiro, wokondweretsa dziko lonse?


Adani ako onse ayasamira pa iwe, atsonya nakukuta mano, nati, Taumeza; ndithu ili ndi tsiku tinaliyembekezalo, talipeza, taliona.


Inde Israele yense walakwira chilamulo chanu, ndi kupatuka, kuti asamvere mau anu; chifukwa chake temberero lathiridwa pa ife, ndi lumbiro lolembedwa m'chilamulo cha Mose mtumiki wa Mulungu; pakuti tamchimwira.


Ndipo anati kwa ine, Ili ndi temberero lilikutulukira padziko lonse; pakuti aliyense wakuba adzapirikitsidwa kuno monga mwa ili; ndi aliyense wakulumbira zonama adzapirikitsidwa kuno monga mwa ili.


Ndipo adzabwezera mitima ya atate kwa ana, ndi mitima ya ana kwa atate ao; kuti ndisafike ndi kukantha dziko lionongeke konse.


Ndipo msonkhano wonse wa ana a Israele unasonkhana ku Silo, nuutsa komweko chihema chokomanako; ndipo dziko linawagonjera.