Koma mukadzabwerera pang'ono pokha osanditsata, kapena inu, kapena ana anu, osasunga malamulo anga ndi malemba anga amene ndawaika pamaso panu; mukadzatumikira milungu ina ndi kuilambira;
Yeremiya 26:4 - Buku Lopatulika Ndipo iwe uziti kwa iwo, Yehova atero: Ngati simudzandimvera Ine kuyenda m'chilamulo changa, chimene ndachiika pamaso panu, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iwe uziti kwa iwo, Yehova atero: Ngati simudzandimvera Ine kuyenda m'chilamulo changa, chimene ndachiika pamaso panu, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ukaŵauze kuti, Chauta akuti: Ngati simundimvera Ine, ngati simutsata malamulo amene ndidakupatsani, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ukawawuze kuti, ‘Yehova akuti: Ngati simundimvera Ine ndi kuleka kutsatira malamulo anga, amene ndakupatsani, |
Koma mukadzabwerera pang'ono pokha osanditsata, kapena inu, kapena ana anu, osasunga malamulo anga ndi malemba anga amene ndawaika pamaso panu; mukadzatumikira milungu ina ndi kuilambira;
koma ngati mukana ndi kupanduka, mudzathedwa ndi lupanga; chifukwa m'kamwa mwa Yehova mwatero.
Koma ngati simudzamvera Ine kulipatula tsiku la Sabata, kusanyamula katundu ndi kulowa pa zipata za Yerusalemu tsiku la Sabata; pamenepo ndidzayatsa moto m'zipata zakezo, ndipo udzatha zinyumba za Yerusalemu, osazimidwanso.
Koma ngati simudzamva mau amenewa, Ine ndilumbira, pali Ine mwini, ati Yehova, nyumba iyi idzakhala yabwinja.
ndipo analowa, nakhalamo; koma sanamvere mau anu, sanayende m'chilamulo chanu; sanachite kanthu ka zonse zimene munawauza achite; chifukwa chake mwafikitsa pa iwo choipa chonsechi;
Sanadzichepetse mpaka lero lomwe, sanaope, sanayende m'chilamulo changa, kapena m'malemba anga, amene ndinaika pamaso panu ndi pa makolo anu.
Chifukwa mwafukiza, ndi chifukwa mwachimwira Yehova, osamvera mau a Yehova, osayenda m'chilamulo chake, ndi m'malemba ake, ndi m'mboni zake, chifukwa chake choipachi chakugwerani, monga lero lomwe.
chifukwa chake ndidzaichitira nyumba iyi, imene itchedwa dzina langa, imene mukhulupirirayi, ndipo ndidzachitira malo amene ndinakupatsani inu ndi makolo anu, monga ndinachitira Silo.
Pakuti nditakalowetsa awa m'dziko limene ndinalumbirira makolo ao, moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ndipo atadya nakhuta, nanenepa, pamenepo adzatembenukira milungu ina, ndi kuitumikira, ndi kundipeputsa Ine, ndi kuthyola chipangano changa.
Ndipo mtundu waukulu wa anthu ndi uti, wakukhala nao malemba ndi maweruzo olungama, akunga chilamulo ichi chonse ndichiika pamaso panu lero lino?
kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, m'mene Mulungu sangathe kunama, tikakhale nacho chotichenjeza cholimba, ife amene tidathawira kuchigwira chiyembekezo choikika pamaso pathu;