Ndi ana a Yosiya: woyamba Yohanani, wachiwiri Yehoyakimu, wachitatu Zedekiya, wachinai Salumu.
Yeremiya 26:1 - Buku Lopatulika Poyamba kukhala mfumu Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, panadza mau awa ochokera kwa Yehova, kuti, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Poyamba kukhala mfumu Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, panadza mau awa ochokera kwa Yehova, kuti, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene Yehoyakimu, mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda, adayamba kulamulira, Chauta adauza Yeremiya kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehoyakimu, mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda atayamba kulamulira, Yehova anayankhula ndi Yeremiya kuti, |
Ndi ana a Yosiya: woyamba Yohanani, wachiwiri Yehoyakimu, wachitatu Zedekiya, wachinai Salumu.
Anamdzeranso masiku a Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, kufikira Zedekiya mwana wake wa Yosiya mfumu ya Yuda atatsiriza zaka khumi ndi chimodzi; kufikira a ku Yerusalemu anatengedwa ndende mwezi wachisanu.
Mau amene anadza kwa Yeremiya za anthu onse a Yuda chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda; ndicho chaka choyamba cha Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni;
Poyamba kukhala mfumu Zedekiya mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, mau awa anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, kuti,
Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova masiku a Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, kuti,
Ndipo panali chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, mau awa anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, kuti,