Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Yeremiya 2:9 - Buku Lopatulika

Chifukwa chake ndidzatsutsananso nanu, ati Yehova, ndi ana a ana anu ndidzatsutsana nao.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Chifukwa chake ndidzatsutsananso nanu, ati Yehova, ndi ana a ana anu ndidzatsutsana nao.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

“Tsono ndidzakuimbanibe mlandu,” akuterotu Chauta. “Ndidzaimbanso mlandu zidzukulu zanu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“Chifukwa chake Ine ndidzakuyimbaninso mlandu,” akutero Yehova. “Ndipo ndidzayimbanso mlandu zidzukulu zanu.

Onani mutuwo



Yeremiya 2:9
12 Mawu Ofanana  

Kumwamba adzaitana zakumwamba, ndi dziko lapansi, kuti aweruze anthu ake.


Usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndili Mulungu wansanje, wakulanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai wa iwo amene akudana ndi Ine;


Yehova aimirira kuti atsutsane, naimiriranso kuti aweruze mitundu ya anthu.


Undikumbutse Ine; tiyeni, tinenane pamodzi; fotokoza mlandu wako, kuti ukalungamitsidwe.


Chifukwa chanji mudzatsutsana ndi Ine nonse? Mwandilakwira Ine, ati Yehova.


Koma unati, Ndili wosachimwa ndithu; mkwiyo wake wachoka pa ine. Taona, ndidzakuweruza iwe, chifukwa uti, Sindinachimwe.


M'mimba anagwira kuchitendeni cha mkulu wake, ndipo atakula mphamvu analimbana ndi Mulungu;


Mutsutsane naye mai wanu, mutsutsane naye; pakuti sali mkazi wanga, ndi Ine sindili mwamuna wake; ndipo achotse zadama zake pankhope pake, ndi zigololo zake pakati pa mawere ake;


Imvani mau a Yehova, inu ana a Israele; pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi okhala m'dziko, popeza palibe choonadi, kapena chifundo, kapena kudziwa Mulungu m'dziko.


pamenepo nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndi banja lake, ndi kumsadza iye, ndi onse akumtsata ndi chigololo kukachita chigololo kwa Moleki, kuwachotsa pakati pa anthu a mtundu wao.


Tamverani, mapiri inu, chitsutsano cha Yehova, ndi inu maziko olimba a dziko lapansi; pakuti Yehova ali nacho chitsutsano ndi anthu ake, ndipo adzatsutsana ndi Israele.