Yeremiya 2:4 - Buku Lopatulika Tamvani mau a Yehova, iwe nyumba ya Yakobo, ndi inu mabanja onse a nyumba ya Israele; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tamvani mau a Yehova, iwe nyumba ya Yakobo, ndi inu mabanja onse a nyumba ya Israele; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu zidzukulu za Yakobe, mabanja onse a Israele, mverani mau a Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Imvani mawu a Yehova, inu zidzukulu za Yakobo, inu mafuko onse a Israeli. |
nuti, Tamvani mau a Yehova, inu mafumu a Yuda, ndi okhala mu Yerusalemu; Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzatengera malo ano choipa, chimene aliyense adzachimva, makutu ake adzachita woo.
Israele anali wopatulikira Yehova, zipatso zoyamba za zopindula zake; onse amene adzamudya iye adzayesedwa opalamula; choipa chidzawagwera, ati Yehova.
atero Yehova, Atate anu apeza chosalungama chanji mwa Ine, kuti andichokera kunka kutali, natsata zachabe, nasanduka achabe?
Nthawi yomweyo, ati Yehova, ndidzakhala Mulungu wa mabanja onse a Israele, ndipo iwo adzakhala anthu anga.
Kodi sulingalira chomwe anena anthu awa, kuti, Mabanja awiri amene Yehova anawasankha, wataya iwo? Chomwecho anyoza anthu anga, kuti asakhalenso mtundu pamaso pao.
Koma tamva mau a Yehova, iwe Zedekiya mfumu ya Yuda; Yehova atero za iwe, Sudzafa ndi lupanga;
Tamvanitu ichi, inu anthu opusa, ndi opanda nzeru; ali ndi maso koma osaona, ali ndi makutu koma osamva;
Ima m'chipata cha nyumba ya Yehova, lalikira m'menemo mau awa, ndi kuti, Tamvani mau a Yehova, inu nonse a Yuda, amene alowa m'zipata izi kuti mugwadire Yehova.
Imvani mau a Yehova, inu ana a Israele; pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi okhala m'dziko, popeza palibe choonadi, kapena chifundo, kapena kudziwa Mulungu m'dziko.
Tamverani tsono chonena Yehova: Nyamuka, tsutsana nao mapiri, ndi zitunda zimve mau ako.