Yeremiya 18:3 - Buku Lopatulika Ndipo ndinatsikira kunyumba ya woumba, ndipo, taonani, anaumba ntchito yake ndi njinga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ndinatsikira kunyumba ya woumba, ndipo, taonani, anaumba ntchito yake ndi njinga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero ndidatsikira ku nyumba ya woumba mbiya, ndipo ndidampeza akuumba mbiya pa mkombero. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho ndinatsikira ku nyumba ya wowumba mbiya, ndipo ndinamuona akuwumba mbiya pa mkombero. |
Ndipo pamene mbiya alikuiumba ndi dothi inaonongeka m'dzanja la woumba, anaiumbanso mbiya ina, monga kunamkomera woumba kuiumba.
Koma Yona ananyamuka kuti athawire ku Tarisisi, kuzemba Yehova; ndipo anatsikira ku Yopa, napezako chombo chomuka ku Tarisisi, napereka ndalama zake, natsikira m'menemo, kuti apite nao ku Tarisisi kuzemba Yehova.