Nthawi imeneyo Yehova ananena ndi Yesaya, mwana wa Amozi, nati, Muka numasule chiguduli m'chuuno mwako, nuchichotse, nuvule nsapato yako kuphazi lako. Ndipo iye anatero, nayenda maliseche, ndi wopanda nsapato.
Yeremiya 18:2 - Buku Lopatulika Tauka, tatsikira kunyumba ya woumba, pamenepo ndidzakumvetsa mau anga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tauka, tatsikira kunyumba ya woumba, pamenepo ndidzakumvetsa mau anga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Nyamuka, upite ku nyumba ya munthu woumba mbiya, kumeneko ukamva mau anga.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Pita ku nyumba ya munthu wowumba mbiya, ndipo kumeneko ndikakuwuza mawu anga.” |
Nthawi imeneyo Yehova ananena ndi Yesaya, mwana wa Amozi, nati, Muka numasule chiguduli m'chuuno mwako, nuchichotse, nuvule nsapato yako kuphazi lako. Ndipo iye anatero, nayenda maliseche, ndi wopanda nsapato.
Atero Yehova kwa ine, Pita, udzigulire mpango wabafuta, nudzimangire m'chuuno mwako, usauike m'madzi.
Ndipo ndinatsikira kunyumba ya woumba, ndipo, taonani, anaumba ntchito yake ndi njinga.
Koma akadaima mu upo wanga, akadamvetsa anthu anga mau anga, akadatembenuza iwo kunjira yao yoipa, ndi kuchoipa cha ntchito zao.
Anandionetsa chotere; ndipo taonani, Ambuye anaima pa khoma lomangidwa ndi chingwe cholungamitsira chilili; ndi chingwe cholungamitsira chilili m'dzanja lake.