Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Yeremiya 16:3 - Buku Lopatulika

Pakuti Yehova atero za ana aamuna ndi za ana aakazi akubadwa m'malo muno, ndi za amai anawabala iwo, ndi za atate ao anawabala iwo m'dziko muno:

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Pakuti Yehova atero za ana amuna ndi za ana akazi akubadwa m'malo muno, ndi za amai anawabala iwo, ndi za atate ao anawabala iwo m'dziko muno:

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ndithu kunena za ana aamuna kapena ana aakazi obadwira kuno, kapenanso za amai ao ndi atate ao amene adabereka anawo m'dziko muno,

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

pakuti ana aamuna ndi ana aakazi obadwira mʼdziko muno, komanso amayi awo ndi abambo awo amene anabereka anawo mʼdziko muno,

Onani mutuwo



Yeremiya 16:3
6 Mawu Ofanana  

Amasiye ao andichulukira Ine kopambana mchenga wa kunyanja; ndatengera wofunkha usana afunkhire mai wao wa anyamata; ndamgwetsera dzidzidzi kuwawa mtima ndi mantha.


Usatenge mkazi, usakhale ndi ana aamuna ndi aakazi m'malo muno.


Pakuti Yehova atero, Usalowe m'nyumba ya maliro, usanke kukachita maliro ao, kapena kuwalirira; pakuti ndachotsa mtendere wanga pa anthu awa, chifundo ndi nsoni zokoma, ati Yehova.


Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele; Taonani, ndidzaletsa pano, pamaso panu masiku anu, mau akukondwerera ndi mau akusangalala, mau a mkwati ndi mau a mkwitibwi.


Chifukwa chake atero Yehova, Taona, ndidzaikira anthuwa zophunthwitsa; ndipo atate ndi ana adzakhumudwa nazo pamodzi; munthu ndi mnzake adzatayika.


Nena ndi nyumba ya Israele, Atero Ambuye Yehova, Taona, ndidzadetsa malo anga opatulika, ulemerero wa mphamvu yanu, chokonda m'maso mwanu, chimene moyo wanu ali nacho chifundo; ndipo ana anu aamuna ndi aakazi otsalira inu adzagwa ndi lupanga.