Pakuti ife tonse takhala ngati wina amene ali wosakonzeka; ndi zolungama zathu zonse zili ngati chovala chodetsedwa; ndipo ife tonse tifota monga tsamba, ndi zoipa zathu zitiuluza monga mphepo.
Yeremiya 13:7 - Buku Lopatulika Ndipo ndinanka ku Yufurate, ndikukumba, nditenga mpango m'malo m'mene ndinaubisamo; ndipo, taonani, mpango unaonongeka, wosayenera kanthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ndinanka ku Yufurate, ndikumba, nditenga mpango m'malo m'mene ndinaubisamo; ndipo, taonani, mpango unaonongeka, wosayenera kanthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ine ndidapita ku Yufurate, ndipo ndidakumba pa malo amene ndidaubisa paja, nkuutenga. Koma ndidaona kuti ndi woonongeka kotheratu, wopandanso ntchito. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho ndinapita ku Yufurate kukafukula lambayo ndi kumuchotsa pamalo pamene ndinamubisa, koma nthawi imeneyi nʼkuti lambayo atawonongeka kotheratu ndipo analibenso ntchito. |
Pakuti ife tonse takhala ngati wina amene ali wosakonzeka; ndi zolungama zathu zonse zili ngati chovala chodetsedwa; ndipo ife tonse tifota monga tsamba, ndi zoipa zathu zitiuluza monga mphepo.
Anthu oipa awa, amene akana kumva mau anga, amene ayenda m'kuumirira kwa mtima wao, atsata milungu ina kuitumikira, ndi kuigwadira, adzakhala ngati mpango uwu, wosayenera kanthu.
Ndipo panali atapita masiku ambiri, kuti Yehova anati kwa ine, Uka, pita ku Yufurate, nukatenge kumeneko mpango uja, ndinakuuza iwe ukaubise kumeneko.
onsewa apatuka, pamodzi akhala opanda pake; palibe mmodzi wakuchita zabwino, inde, palibe mmodzi ndithu.