Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Yeremiya 13:5 - Buku Lopatulika

Ndipo ndinapita, ndinaubisa pa Yufurate, monga Yehova anandiuza ine.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo ndinapita, ndinaubisa pa Yufurate, monga Yehova anandiuza ine.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono ndidapitadi kukaubisa mpangowo ku Yufurate, monga momwe Chauta adaandiwuzira.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndipo ndinapitadi ndi kukabisa lambayo ku Yufurate, monga anenera Yehova.

Onani mutuwo



Yeremiya 13:5
10 Mawu Ofanana  

Anatero Mose; monga mwa zonse Yehova adamuuza, momwemo anachita.


Ndipo panali atapita masiku ambiri, kuti Yehova anati kwa ine, Uka, pita ku Yufurate, nukatenge kumeneko mpango uja, ndinakuuza iwe ukaubise kumeneko.


M'mwemo ndinanenera monga anandiuza, ndipo ponenera ine panali phokoso; ndipo taonani, panali gobedegobede, ndi mafupa anasendererana, fupa kutsata fupa linzake.


Umve zowawa pamodzi nane monga msilikali wabwino wa Khristu Yesu.


Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poitanidwa, anamvera kutuluka kunka kumalo amene adzalandira ngati cholowa; ndipo anatuluka wosadziwa kumene akamukako.