Ku mitsinje ya ku Babiloni, kumeneko tinakhala pansi, inde tinalira, pokumbukira Ziyoni.
Yeremiya 13:4 - Buku Lopatulika Tenga mpango umene unaugula, umene uli m'chuuno mwako, nuuke, nupite ku Yufurate, nuubise m'menemo m'phanga la m'mwala. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tenga mpango umene unaugula, umene uli m'chuuno mwako, nuuke, nupite ku Yufurate, nuubise m'menemo m'phanga la m'mwala. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Tenga mpango uja udagula nkuvala m'chiwuno mwakowu. Unyamuke nkupita msanga ku mtsinje wa Yufurate. Kumeneko ukabise mpangowo m'ming'alu yam'mathanthwe.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Tenga lamba amene unagula ndi kuvala mʼchiwuno mwako uja. Tsono pita ku mtsinje wa Yufurate ndipo ukamubise lambayo mʼmingʼalu ya mʼmatanthwe.” |
Ku mitsinje ya ku Babiloni, kumeneko tinakhala pansi, inde tinalira, pokumbukira Ziyoni.
Imva zowawa, nuyesetse kubala, mwana wamkazi wa Ziyoni, ngati mkazi wakubala; pakuti udzatuluka m'mzinda tsopano, nudzakhala kuthengo, nudzafika ku Babiloni; komweko udzapulumutsidwa; komweko Yehova adzakuombola m'manja a adani ako.
Ndipo Yohane yekhayo anali nacho chovala chake cha ubweya wangamira, ndi lamba lachikopa m'chuuno mwake; ndi chakudya chake chinali dzombe ndi uchi wakuthengo.