Ndipo Yehova anati, Monga mtumiki wanga Yesaya wayenda maliseche ndi wopanda nsapato zaka zitatu, akhale chizindikiro ndi chodabwitsa kwa Ejipito ndi kwa Etiopiya;
Yeremiya 13:1 - Buku Lopatulika Atero Yehova kwa ine, Pita, udzigulire mpango wabafuta, nudzimangire m'chuuno mwako, usauike m'madzi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Atero Yehova kwa ine, Pita, udzigulire mpango wabafuta, nudzimangire m'chuuno mwako, usauike m'madzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adandiwuza kuti, “Pita ukagule mpango wa nsalu yabafuta, ukavale m'chiwuno, koma osakauviika m'madzi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova anandiwuza kuti, “Pita kagule lamba wansalu yosalala ndipo ukavale mʼchiwuno mwako, koma usakamuviyike mʼmadzi.” |
Ndipo Yehova anati, Monga mtumiki wanga Yesaya wayenda maliseche ndi wopanda nsapato zaka zitatu, akhale chizindikiro ndi chodabwitsa kwa Ejipito ndi kwa Etiopiya;
Pakuti monga mpango uthina m'chuuno cha munthu, chomwecho ndinathinitsa kwa Ine nyumba yonse ya Israele ndi nyumba yonse ya Yuda, ati Yehova, kuti akhale kwa Ine anthu, ndi dzina, ndi chilemekezo, ndi ulemerero; koma anakana kumva.
Atero Yehova, Pita, nugule nsupa ya woumba, nutenge akulu a anthu, ndi akulu a ansembe;
Tenga miyala yaikulu m'dzanja lako, nuiyale ndi dothi pakati pa njerwa, za pa khomo la nyumba ya Farao mu Tapanesi pamaso pa anthu a Yuda;
Ndipo anadza kwa ife natenga lamba la Paulo, nadzimanga yekha manja ndi mapazi, nati, Atero Mzimu Woyera, Munthu mwini lamba ili, adzammanga kotero Ayuda a mu Yerusalemu, nadzampereka m'manja a amitundu.