aneneri anenera monyenga nathandiza ansembe pakulamulira kwao; ndipo anthu anga akonda zotere; ndipo mudzachita chiyani pomalizira pake?
Yeremiya 11:9 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova anati kwa ine, Chiwembu chaoneka mwa anthu a Yuda, ndi mwa anthu okhala mu Yerusalemu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova anati kwa ine, Chiwembu chaoneka mwa anthu a Yuda, ndi mwa anthu okhala m'Yerusalemu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kenaka Chauta adandiwuza kuti, “Anthu a ku Yuda ndi anthu a mu Yerusalemu andiwukira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu andiwukira. |
aneneri anenera monyenga nathandiza ansembe pakulamulira kwao; ndipo anthu anga akonda zotere; ndipo mudzachita chiyani pomalizira pake?
Pakuti kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu onse akhala akusirira; ndiponso kuyambira mneneri kufikira wansembe onse achita monyenga.
Chifukwa chake ndidzapereka akazi ao kwa ena, ndi minda yao kwa iwo adzalowamo; pakuti onse kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu asirirasirira; kuyambira mneneri kufikira wansembe onse achita zonyenga.
Ndipo monga magulu a mbala alalira munthu, momwemo msonkhano wa ansembe amapha panjira ya ku Sekemu; indedi achita choipitsitsa.
Akulu ake aweruza chifukwa cha mphotho, ndi ansembe ake aphunzitsa chifukwa cha malipo, ndi aneneri ake alosa chifukwa cha ndalama; koma atsamira pa Yehova, nati, Kodi Yehova sali pakati pa ife? Palibe choipa chodzatigwera.
nati, Mufuna kundipatsa chiyani, ndipo ine ndidzampereka Iye kwa inu? Ndipo iwo anamwerengera iye ndalama zasiliva makumi atatu.