Yeremiya 10:4 - Buku Lopatulika Aukometsa ndi siliva ndi golide; auchirikiza ndi misomali ndi nyundo, kuti usasunthike. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Aukometsa ndi siliva ndi golide; auchirikiza ndi misomali ndi nyundo, kuti usasunthike. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu ena amakongoletsa chosemacho ndi siliva ndi golide, kenaka nkuchikhomerera ndi misomali, kuti chisagwedezeke. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amakongoletsa chosemacho ndi siliva ndi golide; kenaka amachikhomerera ndi misomali kuti chisagwedezeke. |
Wachipala achita zake ndi nsompho, nagwira ntchito ndi makala, nafanizira fanolo ndi nyundo, nagwira ntchito yake ndi mkono wake wamphamvu; inde, ali ndi njala, ndipo mphamvu zake zilephera; iye samwa madzi, nalefuka.
Amene ataya golide, namtulutsa m'thumba, ndi kuyesa siliva ndi muyeso, iwo alemba wosula golide; iye napanga nazo mulungu; iwo agwada pansi, inde alambira.
Iwo amanyamula mlunguwu paphewa, nausenza, naukhazika m'malo mwake, nukhala chilili; pamalo pakepo sudzasunthika; inde, wina adzaufuulira, koma sungathe kuyankha, kapena kumpulumutsa m'zovuta zake.
Ndipo tsopano aonjeza kuchimwa, nadzipangira mafano oyenga a siliva wao, mafano monga mwa nzeru zao, onsewo ntchito ya amisiri; anena za iwo, Anthu ophera nsembe apsompsone anaang'ombe.
Tsoka iye wakunena kwa mtengo, Galamuka; ndi kwa mwala wosalankhula, Nyamuka! Kodi ichi chiphunzitsa? Taona chakutidwa ndi golide ndi siliva, ndi m'kati mwake mulibe mpweya konse.