Ndipo Mulungu anati, Pakhale zounikira pathambo la kumwamba, zakulekanitsa usana ndi usiku; zikhale zizindikiro ndi nyengo, ndi masiku, ndi zaka;
Yeremiya 10:2 - Buku Lopatulika Atero Yehova, Musaphunzire njira ya amitundu, musaope zizindikiro za m'thambo; pakuti amitundu aziopa izo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Atero Yehova, Musaphunzire njira ya amitundu, musaope zizindikiro za m'thambo; pakuti amitundu aziopa izo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta akuti, “Musatsate makhalidwe a anthu a mitundu ina. Musachite mantha ndi zizindikiro zozizwitsa zamumlengalenga, ngakhale anthu a mitundu ina amachita nazo mantha zimenezi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova akuti, “Musatsatire makhalidwe a anthu a mitundu ina kapena kuchita mantha ndi zizindikiro zamlengalenga, ngakhale anthu a mitundu ina amachita nazo mantha. |
Ndipo Mulungu anati, Pakhale zounikira pathambo la kumwamba, zakulekanitsa usana ndi usiku; zikhale zizindikiro ndi nyengo, ndi masiku, ndi zaka;
ndi ichi chimauka mumtima mwanu sichidzachitika, umo mukuti, Tidzakhala ngati amitundu, ngati mabanja a m'maiko, kutumikira mtengo ndi mwala.
Musamachita monga mwa machitidwe a dziko la Ejipito, muja munakhalamo; musamachita monga mwa machitidwe a dziko la Kanani kumene ndipita nanuko, nimusamayenda m'malemba ao.
Musamatsata miyambo ya mtundu umene ndiuchotsa pamaso panu; popeza anachita izi zonse, ndinalema nao.
Mutakalowa m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, musamaphunzira kuchita monga mwa zonyansa za amitundu aja.
ndipo ndinati kwa inu, Ine ndine Yehova Mulungu wanu; musamaopa milungu ya Aamori amene mukhala m'dziko lao; koma simunamvere mau anga.