Yeremiya 10:16 - Buku Lopatulika Gawo la Yakobo silifanana ndi iwo; pakuti Iye ndiye analenga zonse; Israele ndiye mtundu wa cholowa chake; dzina lake ndi Yehova wa makamu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Gawo la Yakobo silifanana ndi iwo; pakuti Iye ndiye analenga zonse; Israele ndiye mtundu wa cholowa chake; dzina lake ndi Yehova wa makamu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Iye uja amene ali choloŵa cha Yakobe sali ngati mafanowo, Iye ndiyedi Mlengi wa zonse. Aisraele ndi anthu ake amene Iye adaŵasankha, dzina lake ndi Chauta Wamphamvuzonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Yehova amene ndi Cholowa cha Yakobo sali ngati mafanowo. Iyeyu ndi Mlengi wa zinthu zonse kuphatikizapo Israeli, mtundu umene anawusankha kuti ukhale anthu ake. Dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse. |
Ndinafuulira kwa inu, Yehova; ndinati, Inu ndinu pothawirapo panga, gawo langa m'dziko la amoyo.
Zakumwamba zinalengedwa ndi mau a Yehova; ndipo ndi mpweya wa m'kamwa mwake khamu lao lonse.
Likatha thupi langa ndi mtima wanga, Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga, ndi cholandira changa chosatha.
Kumbukirani msonkhano wanu, umene munaugula kale, umene munauombola ukhale fuko la cholowa chanu; Phiri la Ziyoni limene mukhalamo.
Ndipo tsopano, ngati mudzamvera mau anga ndithu, ndi kusunga chipangano changa, ndidzakuyesani chuma changa cha padera koposa mitundu yonse ya anthu; pakuti dziko lonse lapansi ndi langa;
Ndipo anati, Ngati ndapeza ufulu tsopano pamaso panu, Ambuye, ayendetu Ambuye pakati pa ife; pakuti awa ndi anthu opulupudza; ndipo mutikhululukire mphulupulu ndi uchimo wathu, ndipo mutilandire tikhale cholowa chanu.
Zonse Yehova anazipanga zili ndi zifukwa zao; ngakhale amphulupulu kuti aone tsiku loipa.
pakuti Yehova wa makamu wadalitsa iwo, ndi kuti, Odalitsika Ejipito anthu anga, ndi Asiriya ntchito ya manja anga, ndi Israele cholowa changa.
Ine ndilenga kuyera ndi mdima, Ine ndilenga mtendere ndi choipa, Ine ndine Yehova wochita zinthu zonse zimenezi.
Ndinakwiyira anthu anga, ndinaipitsa cholowa changa, ndi kuwapereka m'manja ako; koma iwe sunawaonetsere chifundo; wasenzetsa okalamba goli lako lolemera ndithu.
Pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wako, amene ndiutsa nyanja, kuti mafunde ake akokome; Yehova wa makamu ndi dzina lake.
Pakuti Mlengi wako ndiye mwamuna wako; Yehova wa makamu ndiye dzina lake; ndi Woyera wa Israele ndiye Mombolo wako; Iye adzatchedwa Mulungu wa dziko lonse lapansi.
Iye analenga dziko lapansi ndi mphamvu yake, nakhazikitsa dziko lapansi ndi nzeru yake, nayala thambo ndi kuzindikira kwake;
Chifukwa palibe akunga Inu, Yehova; muli wamkulu, ndipo dzina lanu lili lalikulu ndi lamphamvu.
Yehova atero, amene apatsa dzuwa kuti liunikire usana, ndi malemba a mwezi ndi a nyenyezi kuti aunikire usiku, amene atonthoza nyanja, pamene mafunde ake agavira; Yehova wa makamu ndi dzina lake:
amene muchitira chifundo anthu zikwi; nimubwezera mphulupulu ya atate m'chifukwa cha ana ao a pambuyo pao, dzina lake ndi Mulungu wamkulu, wamphamvu, Yehova wa makamu;
Atero Yehova wochita zake, Yehova wolenga zake kuti azikhazikitse; dzina lake ndi Yehova:
Pali Ine, ati Mfumu, dzina lake ndi Yehova wa makamu, ndithu monga Tabori mwa mapiri, monga Karimele pambali pa nyanja, momwemo adzafika.
Mombolo wao ngwa mphamvu; dzina lake Yehova wa makamu: adzawanenera mlandu wao ndithu; kuti apumutse dziko lapansi, nadzidzimutse okhala mu Babiloni.
Gawo la Yakobo silifanafana ndi izo; pakuti Iye ndiye analenga zonse; Israele ndi mtundu wa cholowa chake, dzina lake ndi Yehova wa makamu.
Pakuti taona, Iye amene aumba mapiri, nalenga mphepo, nafotokozera munthu maganizo ake, nasanduliza m'mawa ukhale mdima, naponda pa misanje ya dziko lapansi, dzina lake ndiye Yehova Mulungu wa makamu.
Ndipo Yehova adzalandira cholowa chake Yuda, ngati gawo lake m'dziko lopatulikalo, nadzasankhanso Yerusalemu.