amene anamdzera mau a Yehova masiku a Yosiya mwana wake wa Amoni, mfumu ya Ayuda chaka chakhumi ndi chitatu cha ufumu wake.
Yeremiya 1:4 - Buku Lopatulika Ndipo anadza kwa ine mau a Yehova, kuti, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anadza kwa ine mau a Yehova, kuti, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adandiwuza kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova anayankhula nane kuti, |
amene anamdzera mau a Yehova masiku a Yosiya mwana wake wa Amoni, mfumu ya Ayuda chaka chakhumi ndi chitatu cha ufumu wake.
Anamdzeranso masiku a Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, kufikira Zedekiya mwana wake wa Yosiya mfumu ya Yuda atatsiriza zaka khumi ndi chimodzi; kufikira a ku Yerusalemu anatengedwa ndende mwezi wachisanu.
Ndisanakulenge iwe m'mimba ndinakudziwa, ndipo usanabadwe ndinakupatula iwe; ndinakuika kuti ukhale mneneri wa mitundu ya anthu.
anadzadi mau a Yehova kwa Ezekiele wansembe, mwana wa Buzi, m'dziko la Ababiloni kumtsinje Kebara; ndi pomwepo dzanja la Yehova lidamkhalira.