momwemo adzakhala mau anga amene atuluka m'kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula m'mene ndinawatumizira.
Yeremiya 1:12 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova anati kwa ine, Waona bwino pakuti Ine ndidzadikira mau anga kuwachita. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova anati kwa ine, Waona bwino pakuti Ine ndidzadikira mau anga kuwachita. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adati, “Waona bwino. Ineyo ndikuwonetsetsa kuti zichitikedi zimene ndidanena.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova anandiwuza kuti, “Waona bwino, chifukwa Ine ndikuonetsetsa kuti mawu angawa akwaniritsidwe.” |
momwemo adzakhala mau anga amene atuluka m'kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula m'mene ndinawatumizira.
Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine nthawi yachiwiri, kuti, Uona chiyani? Ndipo ndinati, Ine ndiona mphika wogaduka; ndi pakamwa pake unafulatira kumpoto.
Ndipo Yehova anati kwa ine, Kodi uona chiyani, Yeremiya? Ndipo ndinati, Nkhuyu, nkhuyu zabwino, nzabwino ndithu; zoipazo nzoipa ndithu, zosadyeka poti nzoipa.
Ndipo padzakhala kuti, monga ndayang'anira iwo kuzula ndi kupasula ndi kugwetsa, ndi kuononga ndi kusautsa; momwemo ndidzayang'anira iwo kumangitsa mudzi ndi kubzala, ati Yehova.
Pakuti Ine ndine Yehova, ndidzanena, ndi mau ndidzanenawo adzachitika, osazengerezekanso; pakuti m'masiku anu, nyumba yopanduka inu, ndidzanena mau ndi kuwachita, ati Yehova Mulungu.
Chifukwa chake uziti nao, Atero Ambuye Yehova, Palibe amodzi a mau anga adzazengerezekanso; koma mau ndidzanenawo adzachitika, ati Ambuye Yehova.
Ndipo anati, Amosi uona chiyani? Ndipo ndinati, Dengu la zipatso zamalimwe. Nati Yehova kwa ine, Chitsiriziro chafikira anthu anga Israele, sindidzawalekanso.
Kubwezera chilango nkwanga, kubwezera komwe, pa nyengo ya kuterereka phazi lao; pakuti tsiku la tsoka lao layandika, ndi zinthu zowakonzeratu zifulumira kudza.
Ndipo Yehova anamva mau a kunena kwanu, pamene munanena ndi ine; ndipo Yehova anati kwa ine, Ndidamva mau a kunena kwao kwa anthu awa, amene ananena ndi iwe; chokoma chokhachokha adanenachi.