Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Yakobo 4:16 - Buku Lopatulika

Koma tsopano mudzitamandira m'kudzikuza kwanu; kudzitamandira kulikonse kotero nkoipa.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma tsopano mudzitamandira m'kudzikuza kwanu; kudzitamandira kulikonse kotero nkoipa.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Koma monga zilirimu, mumanyada ndi kudzitama. Kunyada konse kotere nkoipa.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Koma mmene zililimu mumangodzitama ndi kudzikuza. Kudzitama konse kotereku ndi koyipa.

Onani mutuwo



Yakobo 4:16
11 Mawu Ofanana  

Udzitamandiranji ndi choipa, chiphona iwe? Chifundo cha Mulungu chikhala tsiku lonse.


Tapenyani, suyu munthuyu amene sanamuyese Mulungu mphamvu yake; amene anatama kuchuluka kwa chuma chake, nadzilimbitsa m'kuipsa kwake.


Monga mitambo ndi mphepo popanda mvula, momwemo ndiye wodzikweza ndi zipatso zake monyenga.


Usanyadire zamawa, popeza sudziwa tsiku lina lidzabala chiyani?


Pakuti wakhulupirira zoipa zako, wati, Palibe wondiona ine; nzeru zako ndi chidziwitso chako zakusandutsa woipa; ndipo wanena mumtima mwako, Ndine, ndipo popanda ine palibenso wina.


Kudzitamanda kwanu sikuli bwino. Kodi simudziwa kuti chotupitsa pang'ono chitupitsa mtanda wonse?


Koma mukakhala nako kaduka kowawa, ndi chotetana m'mtima mwanu, musadzitamandira, ndipo musamanama potsutsana nacho choonadi.


Pakuti chilichonse cha m'dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma kudziko lapansi.


Monga momwe unadzichitira ulemu, nudyerera, momwemo muuchitire chouzunza ndi chouliritsa maliro: pakuti unena mumtima mwake, Ndikhala ine mfumu, wosati wamasiye ine, wosaona maliro konse ine.