Yakobo 4:12 - Buku Lopatulika Woika lamulo ndi woweruza ndiye mmodzi, ndiye amene akhoza kupulumutsa ndi kuononga; koma iwe woweruza mnzako ndiwe yani? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Woika lamulo ndi woweruza ndiye mmodzi, ndiye amene akhoza kupulumutsa ndi kuononga; koma iwe woweruza mnzako ndiwe yani? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mulungu yekha ndiye wopanga Malamulo ndiponso woweruza. Ndiyenso wotha kupulumutsa ndi kuwononga. Nanga iwe ndiwe yani kuti uziweruza mnzako? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pali mmodzi yekha Wopereka Malamulo ndi Woweruza. Ndiye amene akhoza kupulumutsa ndi kuwononga. Kodi ndiwe yani kuti uziweruza mnzako? |
Pakuti Yehova ndiye woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa malamulo, Yehova ndiye mfumu yathu; Iye adzatipulumutsa.
Ndipo musamaopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muope Iye, wokhoza kuononga moyo ndi thupi lomwe muGehena.
Koma ndidzakulangizani amene muzimuopa; taopani Iye amene atatha kupha ali ndi mphamvu yakutaya ku Gehena, inde, ndinena ndinu opani ameneyo.
Chifukwa chake tisaweruzanenso wina mnzake; koma weruzani ichi makamaka, kuti munthu asaike chokhumudwitsa panjira ya mbale wake, kapena chomphunthwitsa.
Ndani iwe wakuweruza mnyamata wa mwini wake? Iye aimirira kapena kugwa kwa mbuye wake wa mwini yekha. Ndipo adzaimiritsidwa; pakuti Ambuye ali wamphamvu kumuimiritsa.
Chifukwa chake uli wopanda mau owiringula, munthu iwe, amene uli yense wakuweruza; pakuti m'mene uweruza wina, momwemo udzitsutsa iwe wekha, pakuti iwe wakuweruza, umachita zomwezo.
Koma munthu iwe, ndiwe yani wakubwezera Mulungu mau? Kodi chinthu chopangidwa chidzanena ndi amene anachipanga, Undipangiranji ine chotero?
kuchokera komweko akhoza kupulumutsa konsekonse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye, popeza ali nao moyo wake chikhalire wa kuwapembedzera iwo.
Musaipidwe wina ndi mnzake, abale, kuti mungaweruzidwe. Taonani, woweruza aima pakhomo.
Koma Nabala anayankha anyamata a Davide nati, Davide ndani? Ndi mwana wa Yese ndani? Masiku ano pali anyamata ambiri akungotaya ambuye ao.