Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Yakobo 3:4 - Buku Lopatulika

Taonani, zombonso, zingakhale zazikulu zotere, nkutengedwa ndi mphepo zolimba, zipotozeka ndi tsigiro laling'ono ndithu kumene kulikonse afuna wogwira tsigiro.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Taonani, zombonso, zingakhale zazikulu zotere, nizitengedwa ndi mphepo zolimba, zipotozeka ndi tsigiro laling'ono ndithu kumene kulikonse afuna wogwira tsigiro.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Onaninso zombo. Ngakhale nzazikulu kwambiri, ndipo zimakankhidwa ndi mphepo yamphamvu, komabe tsigiro laling'onong'ono ndi limene limaziwongolera kulikonse kumene woyendetsa akufuna.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Taonani sitima zapamadzi. Ngakhale ndi zazikulu kwambiri ndipo zimakankhidwa ndi mphepo yamphamvu, zimawongoleredwa ndi tsigiro lalingʼono kulikonse kumene woyendetsayo akufuna kupita.

Onani mutuwo



Yakobo 3:4
8 Mawu Ofanana  

Koma Yehova anautsa chimphepo chachikulu panyanja, ndipo panali namondwe wamkulu panyanja, ndi chombo chikadasweka.


Zinthu zonse zinaperekedwa kwa Ine ndi Atate wanga; ndipo palibe munthu adziwa Mwana, koma Atate yekha, ndi palibe wina adziwa Atate, koma Mwana yekha, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira.


Ndipo onani, panauka namondwe wamkulu panyanja, kotero kuti ngalawa inafundidwa ndi mafunde: koma Iye anali m'tulo.


Koma kenturiyo anakhulupirira watsigiro ndi mwini ngalawa makamaka, wosasamala mau a Paulo.


Koma ngati tiikira akavalo zogwirira m'kamwa mwao atimvere, tipotolozanso thupi lao lonse.


Kotero lilimenso lili chiwalo chaching'ono, ndipo lidzikuzira zazikulu. Taonani, kamoto kakang'ono kayatsa nkhuni zambiri!