Chifukwa cha kundizazira kwako, ndi popeza kudzikuza kwako kwandifikira m'makutu mwanga, ndidzakukowa ndi ngowe yanga m'mphuno mwako, ndi cham'kamwa changa m'milomo mwako; ndipo ndidzakubwezera panjira unadzerayi.
Yakobo 3:3 - Buku Lopatulika Koma ngati tiikira akavalo zogwirira m'kamwa mwao atimvere, tipotolozanso thupi lao lonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ngati tiikira akavalo zogwirira m'kamwa mwao atimvere, tipotolozanso thupi lao lonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Timaika kachitsulo m'kamwa mwa kavalo kuti atimvere, ndipo tingathe kumaongolera thupi lake lonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tikayika tizitsulo mʼkamwa mwa akavalo kuti atimvere, timatha kuwongolera thupi lake lonse. |
Chifukwa cha kundizazira kwako, ndi popeza kudzikuza kwako kwandifikira m'makutu mwanga, ndidzakukowa ndi ngowe yanga m'mphuno mwako, ndi cham'kamwa changa m'milomo mwako; ndipo ndidzakubwezera panjira unadzerayi.
Musakhale monga kavalo, kapena ngati bulu, wopanda nzeru; zomangira zao ndizo cham'kamwa ndi chapamutu zakuwakokera, pakuti ukapanda kutero sadzakuyandikiza.
Ndinati, Ndidzasunga njira zanga, kuti ndingachimwe ndi lilime langa. Ndidzasunga pakamwa panga ndi cham'kamwa, pokhala woipa ali pamaso panga.
Chifukwa cha kundikwiyira Ine kwako, ndi popeza kudzikweza kwako kwafika m'makutu mwanga. Ine ndidzaika mbedza yanga m'mphuno mwako, ndi chapakamwa changa m'milomo yako, ndipo ndidzakubweza iwe m'njira yomwe unadzerayo.
Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthuyu nkopanda pake.
Taonani, zombonso, zingakhale zazikulu zotere, nkutengedwa ndi mphepo zolimba, zipotozeka ndi tsigiro laling'ono ndithu kumene kulikonse afuna wogwira tsigiro.