Monga kasupe atulutsa madzi ake, chomwecho atulutsa zoipa zake; chiwawa ndi kufunkha zimveka m'kati mwake; pamaso panga masiku onse pali kulira ndi mabala.
Yakobo 3:11 - Buku Lopatulika Kodi kasupe atulutsira pa uno womwewo madzi okoma ndi owawa? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kodi kasupe atulutsira pa uno womwewo madzi okoma ndi owawa? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kodi kasupe amatulutsa madzi omweka ndi oŵaŵa pa dzenje limodzimodzi? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi madzi abwino ndi a mchere angatuluke pa kasupe mmodzi? |
Monga kasupe atulutsa madzi ake, chomwecho atulutsa zoipa zake; chiwawa ndi kufunkha zimveka m'kati mwake; pamaso panga masiku onse pali kulira ndi mabala.
Mochokera m'kamwa momwemo mutuluka chiyamiko ndi temberero. Abale anga, izi siziyenera kutero.
Kodi mkuyu ukhoza kubala azitona, abale anga, kapena mpesa kubala nkhuyu? Kotero madzi amchere sangathe kutulutsa okoma.