Musamachita chisalungamo pakuweruza mlandu; usamavomereza munthu wosauka, kapena kulemekeza munthu womveka; uweruze mlandu wa munthu mnzako molungama.
Yakobo 2:9 - Buku Lopatulika koma ngati musamala maonekedwe, muchita uchimo, ndipo mutsutsidwa ndi chilamulo monga olakwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 koma ngati musamala maonekedwe, muchita uchimo, ndipo mutsutsidwa ndi chilamulo monga olakwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma mukamaonetsa kukondera, mukuchimwa, ndipo Malamulo a Mulungu akukutsutsani kuti ndinu opalamula. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma mukamaonetsa tsankho mukuchimwa, ndipo ndinu wochimwa monga wophwanya lamulo. |
Musamachita chisalungamo pakuweruza mlandu; usamavomereza munthu wosauka, kapena kulemekeza munthu womveka; uweruze mlandu wa munthu mnzako molungama.
Ndipo atadza Iyeyo, adzatsutsa dziko lapansi za machimo, ndi za chilungamo, ndi za chiweruziro;
Ndani mwa inu anditsutsa Ine za tchimo? Ngati ndinena choonadi, simundikhulupirira Ine chifukwa ninji?
Koma iwo, m'mene anatulukamo amodziamodzi, kuyambira akulu, kufikira otsiriza; ndipo Yesu anatsala yekha, ndi mkazi, alikuima pakati.
Ndipo Petro anatsegula pakamwa pake, nati, Zoona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankho;
chifukwa kuti pamaso pake palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi ntchito za lamulo; pakuti uchimo udziwika ndi lamulo.
Koma ngati onse anenera, ndipo alowamo wina wosakhulupirira kapena wosaphunzira, atsutsidwa ndi onse; aweruzidwa ndi onse;
Musamasamalira munthu poweruza mlandu; ang'ono ndi akulu muwamvere chimodzimodzi; musamaopa nkhope ya munthu; popeza chiweruzo ncha Mulungu; ndipo mlandu ukakukanikani mubwere nao kwa ine, ndidzaumva.
kudzachitira onse chiweruziro, ndi kutsutsa osapembedza onse, pa ntchito zao zonse zosapembedza, ndi pa zolimba zimene ochimwa osapembedza adalankhula pa Iye.