Yakobo 2:4 - Buku Lopatulika kodi simunasiyanitse mwa inu nokha, ndi kukhala oweruza oganizira zoipa? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kodi simunasiyanitsa mwa inu nokha, ndi kukhala oweruza oganizira zoipa? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Limenelotu ndi tsankho pakati pa inu nokhanokha, ndipo inuyo mwasanduka oweruza a maganizo oipa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero kodi simunachite tsankho pakati panu ndi kukhala oweruza a maganizo oyipa? |
Nanga kwa Iye wosasamalira nkhope za akalonga, wosasiyanitsa pakati pa wolemera ndi wosauka? Pakuti onsewo ndiwo ntchito ya manja ake.
Popeza adzaima padzanja lamanja la waumphawi, kumpulumutsa kwa iwo akuweruza koipa moyo wake.
Kodi muli chete ndithu poyenera inu kunena zolungama? Muweruza ana anthu molunjika kodi?
Chifukwa chake Inenso ndakuikani onyozeka ndi ochepseka kwa anthu onse, popeza simunasunge njira zanga, koma munaweruza mwankhope pochita chilamulo.
Koma nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, yosadzikometsera pamaso.
Musamanenerana, abale. Wonenera mbale, kapena woweruza mbale wake, anenera lamulo, naweruza lamulo: koma ngati uweruza lamulo, suli wochita lamulo, komatu woweruza.