Ndipo Eliya anayandikira kwa anthu onse, nati, Mukayikakayika kufikira liti? Ngati Yehova ndiye Mulungu, mtsateni Iye; ngati Baala, mumtsate iyeyo. Ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe anamuyankha.
Yakobo 1:8 - Buku Lopatulika munthu wa mitima iwiri akhala wosinkhasinkha panjira zake zonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 munthu wa mitima iwiri akhala wosinkhasinkha pa njira zake zonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa pakuti iyeyo ndi wa mitima iŵiri, ndi wosakhazikika pa zochita zake zonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iyeyu ndi munthu wa mitima iwiri, wosakhazikika pa zimene akuchita. |
Ndipo Eliya anayandikira kwa anthu onse, nati, Mukayikakayika kufikira liti? Ngati Yehova ndiye Mulungu, mtsateni Iye; ngati Baala, mumtsate iyeyo. Ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe anamuyankha.
Amaopa Yehova, namatumikiranso milungu yao, monga mwa miyambo ya amitundu anawachotsako.
Ndipo amitundu awa anaopa Yehova, natumikira mafano ao osema; ana ao omwe, ndi zidzukulu zao zomwe, monga anachita makolo ao, momwemo iwo omwe mpaka lero lino.
Ndipo Ambuye anati, Popeza anthu awa ayandikira ndi Ine ndi m'kamwa mwao, nandilemekeza ndi milomo yao, koma mtima wao uli kutali ndi Ine, ndi mantha ao akundiopa Ine, ndi lamulo la anthu analiphunzira;
Mtima wao wagawikana, tsopano adzapezeka opalamula, adzapasula maguwa ao a nsembe, nadzaononga zoimiritsa zao.
Diso ndilo nyali ya thupi; chifukwa chake ngati diso lako lili la kumodzi, thupi lako lonse lidzakhala lowalitsidwa.
Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.
Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu. Sambani m'manja, ochimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu.
okhala nao maso odzala ndi chigololo, osakhoza kuleka uchimo, kunyengerera iwo a moyo wosakhazikika; okhala nao mtima wozolowera kusirira; ana a temberero;
monganso m'makalata ake onse pokamba momwemo za izi; m'menemo muli zina zovuta kuzizindikira, zimene anthu osaphunzira ndi osakhazikika apotoza, monganso atero nao malembo ena, ndi kudziononga nao eni.