Yakobo 1:7 - Buku Lopatulika Pakuti asayese munthu uyu kuti adzalandira kanthu kwa Ambuye; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti asayese munthu uyu kuti adzalandira kanthu kwa Ambuye; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Munthu wotere asamaganiza kuti nkudzalandira kanthu kwa Ambuye ai; Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Munthu wotere asayembekezere kulandira kalikonse kuchokera kwa Ambuye. |
Ndipo pamene mutambasula manja anu, ndidzakubisirani inu maso anga; inde pochulukitsa mapemphero anu Ine sindidzamva; manja anu adzala mwazi.
Koma apemphe ndi chikhulupiriro, wosakayika konse; pakuti wokayikayo afanana ndi funde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuwinduka nayo.
Mupempha, ndipo simulandira, popeza mupempha koipa, kuti mukachimwaze pochita zikhumbitso zanu.