Wobwabwada ngati madzi; sudzapambana; chifukwa unakwera pa kama wa atate wako; pamenepo unaipitsapo; anakwera paja ndigonapo.
Yakobo 1:6 - Buku Lopatulika Koma apemphe ndi chikhulupiriro, wosakayika konse; pakuti wokayikayo afanana ndi funde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuwinduka nayo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma apemphe ndi chikhulupiriro, wosakayika konse; pakuti wokayikayo afanana ndi funde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuwinduka nayo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma wopemphayo apemphe mokhulupirira, ndi mosakayika konse. Paja munthu wokayikakayika ali ngati mafunde apanyanja, amene amavunduka ndi kuŵinduka ndi mphepo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma pamene mupempha, muyenera kukhulupirira osakayika, chifukwa amene amakayika ali ngati mafunde pa nyanja amene amawinduka nakankhika ndi mphepo. |
Wobwabwada ngati madzi; sudzapambana; chifukwa unakwera pa kama wa atate wako; pamenepo unaipitsapo; anakwera paja ndigonapo.
Ndipo Petro anamyankha Iye nati, Ambuye, ngati ndinutu, mundiuze ndidze kwa Inu pamadzi.
Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa;
Chifukwa chake ndifuna kuti amunawo apemphere pamalo ponse, ndi kukweza manja oyera, opanda mkwiyo ndi makani.
tigwiritse chivomerezo chosagwedera cha chiyembekezo chathu, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika;
koma wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna Iye.
Musatengedwe ndi maphunzitso a mitundumitundu, ndi achilendo; pakuti nkokoma kuti mtima ukhazikike ndi chisomo; kosati ndi zakudya, zimene iwo adazitsata sanapindule nazo.
ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo Ambuye adzamuukitsa; ndipo ngati adachita machimo adzakhululukidwa kwa iye.
Aphunzitsi onamawo ndiwo akasupe opanda madzi, nkhungu yokankhika ndi mkuntho; amene mdima wakuda bii uwasungikira.