Yakobo 1:10 - Buku Lopatulika ndipo mbale wolemera anyadire pamene atsitsidwa, pakuti adzapita monga duwa la udzu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pakuti adzapita monga duwa la udzu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo mbale wolemera nayenso anyadire pamene Mulungu amtsitsa, pakuti adzatha ngati duŵa la udzu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma olemera anyadire pamene atsitsidwa, chifukwa adzatha ngati duwa lakuthengo. |
Indedi munthu ayenda ngati mthunzi; Indedi avutika chabe: Asonkhanitsa chuma, ndipo sadziwa adzachilandira ndani?
Mau a wina ati, Fuula. Ndipo ndinati, Kodi ndifuule chiyani? Anthu onse ndi udzu, ndi kukoma kwao konse kunga duwa la m'thengo;
Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.
Pakuti zonsezi mkono wanga wazilenga, momwemo zonsezi zinaoneka, ati Yehova; koma ndidzayang'anira munthu uyu amene ali waumphawi, ndi wa mzimu wosweka, nanthunthumira ndi mau anga.
Koma ngati Mulungu aveka chotero udzu wakuthengo, ukhala lero, ndi mawa uponyedwa pamoto, nanga si inu kopambana ndithu, inu akukhulupirira pang'ono?
ndi iwo akuchita nalo dziko lapansi, monga ngati osachititsa; pakuti maonekedwe a dziko ili apita.
Komatu zenizeninso ndiyesa zonse zikhale chitayiko chifukwa cha mapambanidwe a chizindikiritso cha Khristu Yesu Ambuye wanga, chifukwa cha Iyeyu ndinatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadzionjezere Khristu,
Lamulira iwo achuma m'nthawi ino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziwika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo;
inu amene simudziwa chimene chidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthawi, ndi pamenepo ukanganuka.
Popeza, Anthu onse akunga udzu, ndi ulemerero wao wonse ngati duwa la udzu. Udzuwo ungofota, ndi duwa lake lingogwa;
Ndipo dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala kunthawi yonse.