Ndipo anamperekeza kufikira ku Asiya Sopatere mwana wa Piro, wa ku Berea; ndipo a Atesalonika, Aristariko ndi Sekundo; ndi Gayo wa ku Deribe, ndi Timoteo; ndi a ku Asiya, Tikiko ndi Trofimo.
Tito 3:12 - Buku Lopatulika Pamene ndikatuma Aritema kwa iwe, kapena Tikiko, chita changu kudza kwa ine ku Nikopoli: pakuti ndatsimikiza mtima kugonerako nyengo yachisanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamene ndikatuma Aritema kwa iwe, kapena Tikiko, chita changu kudza kwa ine ku Nikopoli: pakuti ndatsimikiza mtima kugonerako nyengo yachisanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndikadzamtuma Aritema kapena Tikiko kwanuko, uchite chotheka kudzandipeza ku Nikopoli, chifukwa ndatsimikiza kuti ndikakhala kumeneko nyengo yachisanu ikubwerayi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndikadzamutuma Artema kapena Tukiko kwanuko, udzayesetse kundipeza ku Nikapoli, chifukwa ndatsimikiza kukhala kumeneko pa nthawi yozizira. |
Ndipo anamperekeza kufikira ku Asiya Sopatere mwana wa Piro, wa ku Berea; ndipo a Atesalonika, Aristariko ndi Sekundo; ndi Gayo wa ku Deribe, ndi Timoteo; ndi a ku Asiya, Tikiko ndi Trofimo.
ndipo kapena ndidzakhalitsa ndi inu, kapenanso kugonera nyengo yachisanu kuti mukandiperekeze ine kumene kulikonse ndipitako.
Koma kuti mukadziwe inunso za kwa ine, zimene ndichita, zinthu zonse adzakuzindikiritsani Tikiko mbale wokondedwayo, ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye;
Zonse za kwa ine adzakuzindikiritsani Tikiko, mbale wokondedwa ndi mtumiki wokhulupirika ndi kapolo mnzanga mwa Ambuye:
Tayesetsa kudza isanadze nyengo yachisanu. Akukupatsa moni Yubulo, ndi Pude, ndi Lino, ndi Klaudia, ndi abale onse.