Tito 2:6 - Buku Lopatulika Momwemonso anyamata uwadandaulire akhale odziletsa; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Momwemonso anyamata uwadandaulire akhale odziletsa; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Momwemonso amuna achinyamata uŵauzitse kuti akhale odzigwira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Momwemonso, uwalimbikitse amuna achichepere kuti akhale odziletsa. |
Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata iwe; mtima wako nukasangalale masiku a unyamata wako, nuyende m'njira za mtima wako, ndi monga maso ako aona; koma dziwitsa kuti Mulungu adzanena nawe mlandu wa zonsezi.
Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako, asanadze masiku oipa, ngakhale zisanayandikire zakazo zakuti udzati, Sindikondwera nazo;
Ndipo kudzachitika m'tsogolo mwake, ndidzatsanulira mzimu wanga pa anthu onse, ndi ana aamuna ndi aakazi adzanenera, akuluakulu anu adzalota maloto, anyamata anu adzaona masomphenya;
Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.
Ndikulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pachiyambi. Ndikulemberani, anyamata, popeza mwamgonjetsa woipayo. Ndakulemberani, ana, popeza mwazindikira Atate.