Koma amasiye aang'ono uwakane; pakuti pamene ayamba kumchitira Khristu chipongwe afuna kukwatiwa;
Tito 2:4 - Buku Lopatulika kuti akalangize akazi aang'ono akonde amuna ao, akonde ana ao, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kuti akalangize akazi aang'ono akonde amuna ao, akonde ana ao, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa kuti choncho athe kuphunzitsa azimai achitsikana kukonda amuna ao ndi ana ao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono atha kulangiza amayi achichepere kukonda amuna awo ndi ana awo. |
Koma amasiye aang'ono uwakane; pakuti pamene ayamba kumchitira Khristu chipongwe afuna kukwatiwa;
Chifukwa chake nditi akwatiwe amasiye aang'ono, nabale ana, naweruzire nyumba, osapatsa chifukwa kwa mdaniyo chakulalatira;
Momwemonso akazi okalamba akhale nao makhalidwe oyenera anthu oyera, osadierekeza, osakodwa nacho chikondi cha pavinyo, akuphunzitsa zokoma;
akhale odziletsa, odekha, ochita m'nyumba mwao, okoma, akumvera amuna a iwo okha, kuti mau a Mulungu angachitidwe mwano.