Tito 2:2 - Buku Lopatulika okalamba akhale odzisunga, olemekezeka, odziletsa, olama m'chikhulupiriro, m'chikondi, m'chipiriro. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 okalamba akhale odzisunga, olemekezeka, odziletsa, olama m'chikhulupiriro, m'chikondi, m'chipiriro. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Uuze amuna achikulire kuti azikhala osaledzera, ochita zachiukulu, a maganizo anzeru, olimba pa chikhulupiriro, pa chikondi ndi pa kusatepatepa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Phunzitsa amuna achikulire kuti akhale osaledzera, aulemu wawo, odziletsa, okhwima mʼchikhulupiriro, mʼchikondi ndi mʼkupirira. |
Sipadzakhalanso khanda la masiku, pena munthu wokalamba osakwanitsa masiku ake; pakuti mwana adzafa wa zaka zana limodzi; ndipo wochimwa pokhala wa zaka zana limodzi adzatemberedwa.
Pali aimvi uziwagwadira, nuchitire ulemu munthu wokalamba; nuope Mulungu wako; Ine ndine Yehova.
Ndipo anadza kwa Yesu, napenya wogwidwa ziwandayo alikukhala pansi, wovala ndi wa nzeru zake zabwino, ndiye amene anali ndi legio; ndipo anaopa iwo.
Ndipo iwo anatuluka kukaona chimene chinachitika; ndipo anadza kwa Yesu, nampeza munthuyo, amene ziwanda zinatuluka mwa iye, alikukhala pansi kumapazi ake a Yesu wovala ndi wa nzeru zake; ndipo iwo anaopa.
Ndipo m'mene anamfotokozera za chilungamo, ndi chidziletso, ndi chiweruziro chilinkudza, Felikisi anagwidwa ndi mantha, nayankha, Pita tsopano; ndipo ndikaona nthawi, ndidzakuitana iwe.
Pakuti ndi chisomo chapatsidwa kwa ine, ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga Mulungu anagawira kwa munthu aliyense muyeso wa chikhulupiriro.
Ukani molungama, ndipo musachimwe; pakuti ena alibe chidziwitso cha Mulungu. Ndilankhula kunyaza inu.
Koma yense wakuyesetsana adzikanizira zonse. Ndipo iwowa atero kuti alandire korona wakuvunda; koma ife wosavunda.
Pakuti ngati tili oyaluka, titero kwa Mulungu; ngati tili a nzeru zathu, titero kwa inu.
Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.
Koma ife popeza tili a usana tisaledzere, titavala chapachifuwa cha chikhulupiriro ndi chikondi; ndi chisoti chili chiyembekezo cha chipulumutso.
achigololo, akuchita zoipa ndi amuna, akuba anthu, amabodza, olumbira zonama, ndipo ngati kuli kena kakutsutsana nacho chiphunzitso cholamitsa;
koma chisomo cha Ambuye wathu chidachulukatu pamodzi ndi chikhulupiriro ndi chikondi chili mwa Khristu Yesu.
kwa Timoteo mwana wanga weniweni m'chikhulupiriro: Chisomo, chifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi kwa Khristu Yesu Ambuye wathu.
koma chitsirizo cha chilamuliro ndicho chikondi chochokera mu mtima woyera ndi m'chikumbu mtima chokoma ndi chikhulupiriro chosanyenga;
Ndipo kuyenera woyang'anira akhale wopanda chilema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wodzisunga, wodziletsa, wolongosoka, wokonda kuchereza alendo, wokhoza kuphunzitsa;
woweruza bwino nyumba yake ya iye yekha, wakukhala nao ana ake omvera iye ndi kulemekezeka konse.
Momwemonso atumiki akhale olemekezeka, osanena pawiri, osamwetsa vinyo, osati a chisiriro chonyansa;
Umboni uwu uli woona. Mwa ichi uwadzudzule mokalipa, kuti akakhale olama m'chikhulupiriro,
komatu wokonda kuchereza alendo, wokonda zokoma, wodziweruza, wolungama, woyera mtima, wodziletsa;
m'zonse udzionetsere wekha chitsanzo cha ntchito zabwino; m'chiphunzitso chako uonetsere chosavunda, ulemekezeko,
koma makamaka ndidandaulira mwa chikondi, pokhala wotere, Paulo nkhalamba, ndipo tsopano wandendenso wa Khristu Yesu;
Mwa ichi, podzimanga m'chuuno, kunena za mtima wanu, mukhale odzisunga, nimuyembekeze konsekonse chisomo chilikutengedwa kudza nacho kwa inu m'vumbulutso la Yesu Khristu;
Koma chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi; chifukwa chake khalani anzeru, ndipo dikirani m'mapemphero;
Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire:
ndi pachizindikiritso chodziletsa; ndi pachodziletsa chipiriro; ndi pachipiriro chipembedzo;