achigololo, akuchita zoipa ndi amuna, akuba anthu, amabodza, olumbira zonama, ndipo ngati kuli kena kakutsutsana nacho chiphunzitso cholamitsa;
Tito 2:1 - Buku Lopatulika Koma iwe, lankhula zimene ziyenera chiphunzitso cholamitsa: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma iwe, lankhula zimene ziyenera chiphunzitso cholamitsa: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma iwe uziphunzitsa zogwirizana ndi chiphunzitso choona. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma iwe uziphunzitsa zogwirizana ndi chiphunzitso choona. |
achigololo, akuchita zoipa ndi amuna, akuba anthu, amabodza, olumbira zonama, ndipo ngati kuli kena kakutsutsana nacho chiphunzitso cholamitsa;
Ngati munthu aphunzitsa zina, wosavomerezana nao mau a moyowo a Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi chiphunzitsocho chili monga mwa chipembedzo:
Gwira chitsanzo cha mau a moyo, amene udawamva kwa ine, mwa chikhulupiriro ndi chikondi chili mwa Khristu Yesu.
wogwira mau okhulupirika monga mwa chiphunzitso, kuti akakhoze kuchenjeza m'chiphunzitso cholamitsa, ndi kutsutsa otsutsana naye.
Okhulupirika mauwa, ndipo za izi ndifuna kuti ulimbitse mau, kuti iwo akukhulupirira Mulungu asamalire akhalebe atsogoleri a ntchito zabwino. Izi nzokoma ndi zopindulitsa anthu;
akalankhula wina, alankhule ngati manenedwe a Mulungu; wina akatumikira, achite ngati mu mphamvu imene Mulungu ampatsa, kuti m'zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu, amene ali nao ulemerero ndi mphamvu kunthawi za nthawi. Amen.