Tito 1:10 - Buku Lopatulika Pakuti alipo ambiri osamvera mau, olankhula zopanda pake, ndi onyenga, makamaka iwo akumdulidwe, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti alipo ambiri osamvera mau, olankhula zopanda pake, ndi onyenga, makamaka iwo akumdulidwe, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Paja pali anthu ambiri osaweruzika, makamaka pakati pa gulu la anthu ochokera ku Chiyuda. Anthu ameneŵa amalankhula nkhani zopanda pake nkumasokeretsa anzao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Paja pali anthu ambiri osaweruzika, makamaka mʼgulu la anthu a mdulidwe, oyankhula nkhani zopanda pake ndi kusocheretsa anzawo. |
Ndipo anadza ena akutsika ku Yudeya, nawaphunzitsa abale, nati, Mukapanda kudulidwa monga mwambo wa Mose, simungathe kupulumuka.
Popeza tamva kuti ena amene anatuluka mwa ife anakuvutani ndi mau, nasocheretsa mitima yanu; amenewo sitinawalamulire;
ndicho chifukwa cha abale onyenga olowezedwa m'tseri, amene analowa m'tseri kudzazonda ufulu wathu umene tili nao mwa Khristu Yesu, kuti akatichititse ukapolo.
Agalatiya opusa inu, anakulodzani ndani, inu amene Yesu Khristu anaonetsedwa pamaso panu, wopachikidwa?
Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa;
kapena asasamale nkhani zachabe, ndi mawerengedwe osalekeza a mafuko a makolo, ndiwo akuutsa mafunso, osati za udindo wa Mulungu umene uli m'chikhulupiriro;
podziwa ichi, kuti lamulo siliikika kwa munthu wolungama, koma kwa osaweruzika ndi osamvera lamulo, osapembedza, ndi ochimwa, osalemekeza ndi amnyozo, akupha atate ndi akupha amai, akupha anzao,
ngati wina ali wopanda chilema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wokhala nao ana okhulupirira, wosasakaza zake, kapena wosakana kumvera mau.
Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthuyu nkopanda pake.
Ana inu, ndi nthawi yotsiriza iyi; ndipo monga mudamva kuti wokana Khristu akudza, ngakhale tsopano alipo okana Khristu ambiri; mwa ichi tizindikira kuti ndi nthawi yotsirizira iyi.
Iye wakunena kuti, Ndimdziwa Iye, koma wosasunga malamulo ake, ali wabodza, ndipo mwa iye mulibe choonadi;
Okondedwa, musamakhulupirira mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ichokera mwa Mulungu: popeza aneneri onyenga ambiri anatuluka kulowa m'dziko lapansi.
Komatu ndili nazo zinthu pang'ono zotsutsana ndi iwe, popeza uli nao komweko akugwira chiphunzitso cha Balamu, amene anaphunzitsa Balaki aponye chokhumudwitsa pamaso pa ana a Israele, kuti adye zoperekedwa nsembe kwa mafano, nachite chigololo.