pamenepo mkazi wa mbale wake azimyandikiza pamaso pa akulu, nachotse nsapato yake ku phazi la mwamunayo, ndi kumthira malovu pankhope pake, ndi kumyankha ndi kuti, Atere naye mwamuna wosamanga nyumba ya mbale wake.
Rute 4:8 - Buku Lopatulika Ndipo woombolayo anati kwa Bowazi, Udzigulire wekha kadzikoko. Navula nsapato yake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo woombolayo anati kwa Bowazi, Udzigulire wekha kadzikoko. Navula nsapato yake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho pamene wachibale uja adauza Bowazi kuti, “Gulani ndinu mundawo,” adavula nsapato yake napatsa Bowazi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho wachibale uja atawuza Bowazi kuti, “Gulani ndinu mundawu.” Iye anavula nsapato yake namupatsa Bowazi. |
pamenepo mkazi wa mbale wake azimyandikiza pamaso pa akulu, nachotse nsapato yake ku phazi la mwamunayo, ndi kumthira malovu pankhope pake, ndi kumyankha ndi kuti, Atere naye mwamuna wosamanga nyumba ya mbale wake.
Koma kale mu Israele pakuombola ndi pakusinthana, kutsimikiza mlandu wonse, akatero: munthu avula nsapato yake, naipereka kwa mnansi wake; ndiwo matsimikizidwe mu Israele.
Nati Bowazi kwa akulu, ndi kwa anthu onse, Inu ndinu mboni lero lino kuti ndagula zonse za Elimeleki, ndi zonse za Kilioni, ndi Maloni, padzanja la Naomi.