Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Rute 4:5 - Buku Lopatulika

Nati Bowazi, Tsiku lomwelo ugula mundawo padzanja la Naomi, uugulanso kwa Rute, Mmowabu, mkazi wa wakufayo, kuukitsira dzina la wakufayo pa cholowa chake.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Nati Bowazi, Tsiku lomwelo ugula mundawo pa dzanja la Naomi, uugulanso kwa Rute, Mmowabu, mkazi wa wakufayo, kuukitsira dzina la wakufayo pa cholowa chake.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono Bowazi adamuuza kuti, “Tsiku limene udzagule mundawo kwa Naomi, udzatenganso Rute Mmowabu, mai wamasiye uja, kuti dzina la malemu aja lisungike pa choloŵa chao.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Tsono Bowazi anati, “Tsiku limene ukagule mundawo kwa Naomi, udzatenganso Rute Mmowabu, mkazi wamasiye uja, kuti dzina la malemu lisungike pa cholowa chake.”

Onani mutuwo



Rute 4:5
6 Mawu Ofanana  

Ndipo Yuda anati kwa Onani, Lowani naye mkazi wa mbale wako, ndi kumchitira mkazi zoyenera mphwake wa mwamuna wake, ndi kumuukitsira mkulu wako mbeu.


nanena, Mphunzitsi, Mose anati, Ngati munthu akafa wopanda mwana, mphwake adzakwatira mkazi wake, nadzamuukitsira mbale wake mbeu.


nanena, Mphunzitsi, Mose anatilembera ife, kuti mbale wake wa munthu akafa, wokhala ndi mkazi, ndipo alibe mwana iye, mbale wake adzakwatira mkaziyo, nadzamuukitsira mbale wake mbeu.


Ndipo ngati mwamunayo safuna kutenga mkazi wa mbale wake, mkazi wa mbale wakeyo azikwera kunka kuchipata, kwa akulu, ndi kuti, Mbale wa mwamuna wanga akana kuutsira mbale wake dzina mu Israele; safuna kundichitira ine zoyenera mbale wa mwamuna.