Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Rute 4:3 - Buku Lopatulika

Pamenepo anati kwa woombolerayo, Naomi anabwerayo ku dziko la Mowabu ati agulitse kadziko kaja kadali ka mbale wathu Elimeleki;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Pamenepo anati kwa woombolerayo, Naomi anabwerayo ku dziko la Mowabu ati agulitse kadziko kaja kadali ka mbale wathu Elimeleki;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono adauza munthu wachibale uja kuti, “Naomi amene wabwerera kuchokera ku dziko la Mowabu, akugulitsa munda umene udaali wa malemu Elimeleki, wachibale wathu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kenaka anamuwuza oyenera kulowa chokolo uja kuti, “Naomi amene wabwera kuchoka ku Mowabu akugulitsa malo amene anali a malemu Elimeleki, mʼbale wathu uja.

Onani mutuwo



Rute 4:3
5 Mawu Ofanana  

Wodala munthu wakuchitira chifundo, nakongoletsa; adzalimbika nao mlandu wake poweruzidwa.


Kudzikuza kupikisanitsa; koma omwe anauzidwa uphungu ali ndi nzeru.


Taonani, Hanamele mwana wa Salumu mbale wa atate wako adzadza kwa iwe, kuti, Ugule munda wanga uli ku Anatoti; pakuti mphamvu yakuombola ndi yako kuugula.


Mbale wako akasaukira chuma, nakagulitsa chakechake, pamenepo mombolo wake, mbale wake weniweni azidza, naombole chimene mbale wake anagulitsacho.


Dzina la munthuyo ndiye Elimeleki, ndi dzina la mkazi wake ndiye Naomi, ndi maina a ana ake awiri ndiwo Maloni, ndi Kilioni; ndiwo Aefurati a ku Betelehemu ku Yuda. Iwowa ndipo analowa m'dziko la Mowabu, nakhala komweko.