Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Rute 4:2 - Buku Lopatulika

Ndipo anatenga amuna khumi a akulu a mzinda, nati, Mukhale pansi apa. Nakhala pansi iwo.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo anatenga amuna khumi a akulu a mudzi, nati, Mukhale pansi apa. Nakhala pansi iwo.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Adaitananso atsogoleri khumi amumzindamo naŵauza kuti, “Takhalani pansi apa.” Iwo adakhala pansi.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Bowazi anayitananso akuluakulu khumi a mu mzindamo nati, “Dzakhaleni pansi apa,” ndipo anadzakhala pansi.

Onani mutuwo



Rute 4:2
9 Mawu Ofanana  

M'mwemo analemba makalata m'dzina la Ahabu nakhomerapo chizindikiro chake, natumiza makalatawo kwa akulu ndi omveka anali m'mzinda mwake, nakhala naye, Naboti.


Akapanda kumkonda mbuye wake, amene anamtoma mwini yekha, azilola kuti amuombole; alibe mphamvu yakumgulitsa kwa anthu achilendo, popeza wachita naye monyenga.


Mwamuna wake adziwika kubwalo, pokhala pakati pa akulu a dziko.


Akulu adatha kuzipata, anyamata naleka nyimbo zao.


Ndipo anautsa anthu, ndi akulu, ndi alembi, namfikira, namgwira iye, nadza naye kubwalo la akulu a milandu,


Ndipo ngati mwamunayo safuna kutenga mkazi wa mbale wake, mkazi wa mbale wakeyo azikwera kunka kuchipata, kwa akulu, ndi kuti, Mbale wa mwamuna wanga akana kuutsira mbale wake dzina mu Israele; safuna kundichitira ine zoyenera mbale wa mwamuna.


Muimirira inu nonse lero lino pamaso pa Yehova Mulungu wanu; mafumu anu, mafuko anu, akulu anu, ndi akapitao anu, amuna onse a Israele,


Ndisonkhanitsire akulu onse a mafuko anu, ndi akapitao anu, kuti ndinene mau awa m'makutu mwao, ndi kuchititsa mboni kumwamba ndi dziko lapansi zitsutse iwo.