Estere sadawulule mtundu wake ndi chibale chake; pakuti Mordekai adamuuzitsa kuti asadziwulule.
Rute 3:6 - Buku Lopatulika Pamenepo anatsikira popunthirapo, nachita zonse monga umo mpongozi wake adamuuza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo anatsikira popunthirapo, nachita zonse monga umo mpongozi wake adamuuza. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho Rute adapita kopunthira kuja, ndipo adakachitadi monga momwe mpongozi wake uja adaamuuzira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Rute anapita ku malo opunthirawo ndipo anachita monga momwe apongozi ake anamuwuza. |
Estere sadawulule mtundu wake ndi chibale chake; pakuti Mordekai adamuuzitsa kuti asadziwulule.
Uzilemekeza atate wako ndi amai ako; kuti achuluke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.
Ndipo atatha Bowazi kudya ndi kumwa, nusekerera mtima wake, anakagona kuthungo kwa mulu wa tirigu; nadza iye kachetechete, navundukula ku mapazi ake, nagona.