Rute 3:4 - Buku Lopatulika Ndipo kudzali, akagona, upenye apo ati agone, numuke, nuvundukule ku mapazi ake, nugone, ndi iyeyo adzakufotokozera zoyenera kuchita iwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kudzali, akagona, upenye apo ati agone, numuke, nuvundukule ku mapazi ake, nugone, ndi iyeyo adzakufotokozera zoyenera kuchita iwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene akukagona, ukaonetsetse malo amene akagonewo. Tsono ukavundukule chofunda chake nukagona ku mapazi ake. Motero iyeyo akakuuza zoti uchite.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Akamakagona, iwe ukaonetsetse malo amene wagonawo. Kenaka upite ndi kuvundukula chofunda ku mapazi ake ndi kugona. Iyeyo akakuwuza zoti uchite.” |
Usambe tsono, nudzole, nuvale zovala zako, nutsikire popunthirapo, koma usadziwike naye munthuyo, koma atatha kudya ndi kumwa ndiko.