Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Rute 3:2 - Buku Lopatulika

Nanga Bowazi wodziwana nafe, amene unakhala nao adzakazi ake? Taona, usiku uno apuntha barele popunthirapo.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Nanga Bowazi wodziwana nafe, amene unakhala nao adzakazi ake? Taona, usiku uno apuntha barele popunthirapo.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Bowazi amene adzakazi ake unali nawo, ndi wachibale wathu. Usiku uno iye akhala akupuntha barele ku malo ake opunthira.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Bowazi amene adzakazi ake wakhala nawo nthawi yonseyi, si wachibale wathu kodi? Usiku uno akhala akupeta barele ku malo opunthira.

Onani mutuwo



Rute 3:2
8 Mawu Ofanana  

Ndipo anafika pa dwale la Atadi, lili tsidya lija la Yordani, pamenepo anamlira maliro a atate wake masiku asanu ndi limodzi.


Ndipo Naomi anali naye mbale wa mwamuna wake, ndiye munthu mwini chuma chambiri wa banja la Elimeleki; dzina lake ndiye Bowazi.


Pamenepo Bowazi ananena ndi Rute, Ulikumva, mwana wanga? Usakakhunkha m'munda mwina, kapena kupitirira pano, koma uumirire adzakazi anga mommuno.


Pamenepo Naomi mpongozi wake ananena naye, Mwana wanga, kodi ndisakufunire popumulako, kuti ukhale bwino?


Usambe tsono, nudzole, nuvale zovala zako, nutsikire popunthirapo, koma usadziwike naye munthuyo, koma atatha kudya ndi kumwa ndiko.