Pamenepo anyamata ake anasendera, nanena naye, nati, Atate wanga, mneneri akadakuuzani chinthu chachikulu, simukadachichita kodi? Koposa kotani nanga ponena iye, Samba, nukonzeke?
Rute 2:8 - Buku Lopatulika Pamenepo Bowazi ananena ndi Rute, Ulikumva, mwana wanga? Usakakhunkha m'munda mwina, kapena kupitirira pano, koma uumirire adzakazi anga mommuno. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Bowazi ananena ndi Rute, Ulikumva, mwana wanga? Usakakhunkha m'munda mwina, kapena kupitirira pano, koma uumirire adzakazi anga mommuno. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Bowazi adauza Rute kuti, “Tamvera, mwana wanga, usapite kukakunkha ku munda wina, usasiye munda uno, koma uzitsata adzakazi angaŵa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Bowazi anati kwa Rute, “Tamvera mwana wanga, usapite kukakunkha mʼmunda wina, ndipo usachoke mʼmunda uno. Koma uzitsata adzakazi angawa. |
Pamenepo anyamata ake anasendera, nanena naye, nati, Atate wanga, mneneri akadakuuzani chinthu chachikulu, simukadachichita kodi? Koposa kotani nanga ponena iye, Samba, nukonzeke?
Pakukolola dzinthu za m'dziko mwanu, usamakololetsa m'mphepete mwa munda wako, nusamakunkha khunkha.
Ndipo onani, anabwera naye kwa Iye munthu wamanjenje, wakugona pamphasa: ndipo Yesu pakuona chikhulupiriro chao, anati kwa wodwalayo, Limba mtima, mwana, machimo ako akhululukidwa.
Koma Yesu potembenuka ndi kuona iye anati, Limba mtima, mwana wamkaziwe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Ndipo mkaziyo anachira kuyambira nthawi yomweyo.
Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.
ndipo anati, Undilole, ndikunkhe ndiole pakati pa mitolo potsata ochekawo; nadza iye nakhalakhala kuyambira m'mawa mpaka tsopano; koma m'nyumba samakhalitsamo.
Maso ako akhale pamunda achekawo, ndi kuwatsata; kodi sindinawauze anyamata asakukhudze? Ndipo ukamva ludzu, muka kumitsuko, ukamweko otunga anyamatawo,
Ndipo Yehova anabwereza kumuitana, ndi kuti, Samuele. Ndipo Samuele anauka, napita kwa Eli, nati, Ndine, pakuti mwandiitana ndithu. Koma iye anayankha, Sindinaitane, mwana wanga; kagone.