Rute 2:7 - Buku Lopatulika ndipo anati, Undilole, ndikunkhe ndiole pakati pa mitolo potsata ochekawo; nadza iye nakhalakhala kuyambira m'mawa mpaka tsopano; koma m'nyumba samakhalitsamo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo anati, Undilole, ndikunkhe ndiole pakati pa mitolo potsata ochekawo; nadza iye nakhalakhala kuyambira m'mawa mpaka tsopano; koma m'nyumba samakhalitsamo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iyeyu wandipempha kuti, ‘Chonde mundilole kuti ndikunkheko barele m'munda m'mene anthu akolola kale!’ Choncho wakhala akukunkha kuyambira m'mamaŵa mpaka tsopano lino, osapuma ndi pang'ono pomwe.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anandipempha kuti, ‘Chonde mundilole kuti ndikunkhe barele mʼminda moti akololamo kale.’ Iye wakhala akukunkha kuyambira mmawa mpaka tsopano lino osapuma nʼpangʼono pomwe.” |
Kodi upenya munthu wofulumiza ntchito zake? Adzaima pamaso pa mafumu, osaima pamaso pa anthu achabe.
Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.
Nati Rute Mmowabu kwa Naomi, Mundilole ndimuke kumunda, ndikatole khunkha la ngala za tirigu, kumtsata iye amene adzandikomera mtima. Nanena naye, Muka, mwana wanga.
Ndipo Rute Mmowabu anati, Ananenanso nane ndithu, Uwaumirire anyamata anga, mpaka atatha kucheka zanga zonse za m'minda.
Ndipo mnyamata woyang'anira ochekawo anayankha nati, Ndiye mkazi Mmowabuyo anabwera ndi Naomi ku dziko la Mowabu;
Pamenepo Bowazi ananena ndi Rute, Ulikumva, mwana wanga? Usakakhunkha m'munda mwina, kapena kupitirira pano, koma uumirire adzakazi anga mommuno.